pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi.
Genesis 4:13 - Buku Lopatulika Ndipo Kaini anati kwa Yehova, Kulangidwa kwanga nkwakukulu kosapiririka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Kaini anati kwa Yehova, Kulangidwa kwanga nkwakukulu kosapiririka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kaini adauza Chauta kuti, “Chilango chimenechi nchopitirira mphamvu zanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kaini anati kwa Yehova, “Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga. |
pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi.
Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.
nachitira mwano Mulungu wa mu Mwamba chifukwa cha zowawa zao ndi zilonda zao; ndipo sanalape ntchito zao.
Ndipo anatsika kumwamba matalala aakulu, lonse lolemera ngati talente, nagwa pa anthu; ndipo anthu anachitira Mulungu mwano chifukwa cha mliri wa matalala, pakuti mliri wake ndi waukulu ndithu.
Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalape kuti amchitire ulemu.