nundikonzere ine chakudya chokolera chonga chomwe ndichikonda ine, nudze nacho kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe.
Genesis 27:5 - Buku Lopatulika Ndipo anamva Rebeka pamene Isaki ananena ndi Esau mwana wake. Ndipo Esau ananka kuthengo kukasaka nyama ndi kubwera nayo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamva Rebeka pamene Isaki ananena ndi Esau mwana wake. Ndipo Esau ananka kuthengo kukasaka nyama ndi kubwera nayo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Rebeka ankangomvetsera pamene Isaki ankalankhula ndi mwana wake Esau. Tsono Esauyo atapita ku thengo kukasaka nyama yoti akapatse bambo wake, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Rebeka amamvetsera pamene Isake amayankhula ndi mwana wake Esau. Esau atanyamuka kupita kuthengo kukaphera abambo ake nyama, |
nundikonzere ine chakudya chokolera chonga chomwe ndichikonda ine, nudze nacho kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe.
Ndipo Rebeka ananena kwa Yakobo mwana wake, nati, Taona ndinamva atate wako alimkunena ndi Esau mkulu wako kuti,