Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo mu Gerari.
Genesis 26:6 - Buku Lopatulika Ndipo Isaki anakhala mu Gerari; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Isaki anakhala m'Gerari; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Isaki adakhala ku Gerari. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Isake anakhala ku Gerari. |
Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo mu Gerari.
chifukwa kuti Abrahamu anamvera mau anga, nasunga chilangizo changa, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga.
ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.