Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
Genesis 26:26 - Buku Lopatulika Ndipo ananka kwa iye Abimeleki kuchokera ku Gerari, ndi Ahuzati bwenzi lake, ndi Fikolo, kazembe wa nkhondo yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananka kwa iye Abimeleki kuchokera ku Gerari, ndi Ahuzati bwenzi lake, ndi Fikolo, kazembe wa nkhondo yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abimeleki adachoka ku Gerari nabwera kudzacheza ndi Isaki pamodzi ndi Ahuzati, nduna yake, ndi Fikolo mtsogoleri wa ankhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abimeleki pamodzi ndi Ahuzati mlangizi wake ndi Fikolo mkulu wa ankhondo ake anabwera kwa Isake kuchokera ku Gerari. |
Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
Ndipo Isaki anati kwa iwo, Mwandidzera chifukwa chiyani, inu akundida ine, ndi kundichotsa kwanu?