Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m'mene ndinkamo ine;
Genesis 24:41 - Buku Lopatulika ukatero udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abale anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ukatero udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abale anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ukachita zimenezi, matemberero anga sadzakugwera. Koma iweyo utafika ku banja langalo, anthu angawo nakakukana, udzamasuka ku lumbiro lako.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ukadzachita zimenezi udzakhala mfulu wosamangidwa ndi lumbiro langali. Koma tsono ukadzafika kwa fuko langa, ndipo ngati sadzalola kukupatsa mbeta ya mwana wanga, aponso udzamasuka ku lumbiro langali.’ ” |
Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m'mene ndinkamo ine;
Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosachimwa pa chilumbiro changachi: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko.
kuti mulowe chipangano cha Yehova Mulungu wanu, ndi lumbiriro lake, limene Yehova Mulungu wanu achita ndi inu lero lino;