Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
Genesis 2:10 - Buku Lopatulika Ndipo unatuluka mu Edeni mtsinje wakuthirira m'mundamo, m'menemo ndipo unalekana nuchita miyendo inai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo unatuluka m'Edeni mtsinje wakuthirira m'mundamo, m'menemo ndipo unalekana nuchita miyendo inai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtsinje wotuluka mu Edeni momwemo, unkayenda numathirira mundawo. Mtsinjewo udagaŵika panai, nusanduka mitsinje inai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtsinje wothirira mundawo unkatuluka mu Edeni; kuchokera apo unkagawikana kukhala mitsinje inayi. |
Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mzinda wa Mulungu. Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba.
Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.