Ndipo Abrahamu anatenga Ismaele mwana wake ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.
Genesis 17:9 - Buku Lopatulika Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma iwe, uzikumbukira pangano langa, iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma iwe, uzikumbukira pangano langa, iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adauzanso Abrahamu kuti, “Iwenso tsono uyenera kuvomera kusunga chipangano changa, pamodzi ndi zidzukulu zako zam'tsogolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Mulungu anati kwa Abrahamu, “Koma iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako mʼmibado ya mʼtsogolomo, sungani pangano langali. |
Ndipo Abrahamu anatenga Ismaele mwana wake ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.
Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.
Mayendedwe onse a Yehova ndiwo chifundo ndi choonadi, kwa iwo akusunga pangano lake ndi mboni zake.
Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;