Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 15:3 - Buku Lopatulika

Ndipo Abramu anati, Taonani, simunandipatse ine mbeu; ndipo, taonani, wobadwa m'nyumba mwanga adzalowa m'malo mwanga.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Abramu anati, Taonani, simunandipatse ine mbeu; ndipo, taonani, wobadwa m'nyumba mwanga adzalowa m'malo mwanga.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Simudandipatse ana, motero mmodzi mwa akapolo anga ndiye amene adzalandire chuma changa kuti chikhale choloŵa chake.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Inu simunandipatse ana kotero kuti wantchito wa ku nyumba kwanga ndiye amene adzalowe mʼmalo mwanga.”

Onani mutuwo



Genesis 15:3
10 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;


Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa.


Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani.


Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine chiyani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliyezere wa ku Damasiko?


Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima; koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.


Yemwe alera kapolo wake mwa ufulu kuyambira ubwana wake, pambuyo pake adzadziyesa mwana wobala.


chifukwa cha mkazi wodedwa wokwatidwa; ndi mdzakazi amene adzalandira cholowa cha mbuyake.


ndinadzitengera akapolo ndi adzakazi, ndinali ndi akapolo anabadwa kwanga; ndinalemeranso pokhala nazo zoweta zazikulu ndi zazing'ono kupambana onse anakhala mu Yerusalemu ndisanabadwe ine;


Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?