Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga.
Genesis 12:12 - Buku Lopatulika ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aejipito, adzati, Uyu ndi mkazi wake: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aejipito, adzati, Uyu ndi mkazi wake: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Aejipito akakupenya, aziti, ‘Ameneyu ndi mkazi wake,’ tsono kuti akukwatire iwe, andipha ineyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Aigupto akakuona adzanena kuti ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Tsono adzandipha ine nakusiya iwe ndi moyo. |
Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga.
ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.
Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.
Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake.