ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza khumi ndi zisanu ndi zinai, atabala Tera, nabala ana aamuna ndi aakazi.
Genesis 11:26 - Buku Lopatulika Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tera ali wa zaka 70, adabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. |
ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza khumi ndi zisanu ndi zinai, atabala Tera, nabala ana aamuna ndi aakazi.
Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu ina iwowa.