Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 24:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu ina iwowa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu ina iwowa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adauza anthu onsewo kuti, “Zimene Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena ndi izi, akuti, ‘Kale makolo anu ankakhala pa mbali ina ya mtsinje wa Yufurate, ndi kumapembedza milungu ina. Mmodzi mwa makolo ameneŵa anali Tera, bambo wa Abrahamu ndi Nahori.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yoswa anati kwa anthu onse, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Kalekale makolo anu, kuphatikiza Tera, abambo a Abrahamu ndi Nahori ankakhala kutsidya kwa Mtsinje ndipo ankapembedza milungu ina.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 24:2
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Nahori:


Ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka makumi awiri kudza zisanu ndi zinai, nabala Tera:


Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harani.


Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti.


Ndipo Labani ananka kukasenga nkhosa zake: ndipo Rakele anaba aterafi a atate wake.


Tsono ungakhale ukadamuka chifukwa mtima wako ulinkukhumba nyumba ya atate wako, bwanji waba iwe milungu yanga?


Aliyense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi moyo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako zili ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.


Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isaki.


Ndipo anampatsa Yakobo milungu yachilendo yonse inali m'manja mwao, ndi mphete zinali m'makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu.


Abramu, (ndiye Abrahamu).


Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumchulukitsa.


Atero Ambuye Yehova kwa Yerusalemu, Chiyambi chako ndi kubadwa kwako ndiko kudziko la Akanani; atate wako anali Mwamori, ndi mai wako Muhiti.


mwana wa Yakobo, mwana wa Isaki, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nahori,


Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye Mwaramu wakuti atayike, natsika kunka ku Ejipito, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukulu, wamphamvu, ndi wochuluka anthu ake;


Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa