Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.
Genesis 10:20 - Buku Lopatulika Amenewa ndi ana aamuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amenewa ndi ana amuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ameneŵa ndiwo ana a Hamu ndipo ankakhala m'mafuko osiyanasiyana, ndi m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo. |
Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.