Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 1:25 - Buku Lopatulika

Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wake, ndi zonse zokwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wake, ndi zonse zokwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pomwepo Mulungu adalenga nyama zakuthengo potsata mitundu yake, ndi nyama zoŵeta potsata mitundu yake, ndiponso zokwaŵa zonse potsata mitundu yake. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mulungu anapanga nyama zakuthengo monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo ndi nyama zokwawa monga mwa mitundu yawo. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.

Onani mutuwo



Genesis 1:25
9 Mawu Ofanana  

Ndipo zinafa zamoyo zonse zoyenda padziko lapansi, zouluka, ndi nyama, ndi zamoyo, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi, ndi anthu onse:


zonse zimene m'mphuno zao munali mpweya wa mzimu wa moyo, zonse zinali pamtunda, zinafa.


Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza, ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza.


Mwa mzimu wake anyezimiritsa thambo; dzanja lake linapyoza njoka yothawayo.


Sindikhala chete osatchula ziwalo za ng'onayo, ndi mbiri ya mphamvu yake, ndi makonzedwe ake okoma.


Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikulu ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.


pakuti kayeretsedwa ndi Mau a Mulungu ndi kupemphera.