Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ake onse, Onani, mwana wanga wotuluka m'matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? Mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza.
Filemoni 1:12 - Buku Lopatulika amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weniweni wa ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weniweni wa ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikumtumizanso kwa iwe tsopano, ndipo pakutero ndikuchita ngati kukutumizira mtima wanga womwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndikumutumizanso kwa iwe tsopano, koma potero ndikukhala ngati ndikutumiza mtima wanga weniweni. |
Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ake onse, Onani, mwana wanga wotuluka m'matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? Mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza.
Kodi Efuremu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? Nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamchitiradi chifundo, ati Yehova.
Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu.
Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanuwanu, akakukakamizani m'tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu ina, imene simunaidziwe, inu, kapena makolo anu;
Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m'malo mwako akadanditumikira ine m'ndende za Uthenga Wabwino: