Eksodo 9:17 - Buku Lopatulika Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ukunyozabe anthu anga, osafuna kuŵalola kuti apite. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komabe iwe ukudzitukumula pa anthu anga osawalola kuti atuluke. |
Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu; ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?
Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa padziko lonse lapansi.
Taona, mawa monga nthawi ino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhale unzake mu Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.
Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo.
Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.
Chifukwa cha kundikwiyira Ine kwako, ndi popeza kudzikweza kwako kwafika m'makutu mwanga. Ine ndidzaika mbedza yanga m'mphuno mwako, ndi chapakamwa changa m'milomo yako, ndipo ndidzakubweza iwe m'njira yomwe unadzerayo.
Tsoka kwa iye amene akangana ndi Mlengi wake! Phale mwa mapale a dziko lapansi! Kodi dongo linganene kwa iye amene aliumba, Kodi upanga chiyani? Pena ntchito yako, Iye alibe manja?
Koma pokwezeka mtima wake, nulimba mzimu wake kuchita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wake, namchotsera ulemerero wake;
Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatse Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.