Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 9:10 - Buku Lopatulika

Ndipo anatenga phulusa la m'ng'anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zilonda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anatenga phulusa la m'ng'anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zilonda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choncho Mose adatapa phulusalo pa moto ndipo adakaimirira pamaso pa Farao. Adawaza phulusalo kumwamba, ndipo padabuka zithupsa zimene zidaphulika ndi kusanduka zilonda pa anthu ndi pa nyama zomwe.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kotero anatenga phulusa la pa moto ndi kuyima pamaso pa Farao. Mose analiwaza mmwamba, ndipo panabuka zotupa zophulika zokha pa munthu aliyense ndi pa ziweto.

Onani mutuwo



Eksodo 9:10
4 Mawu Ofanana  

Ndipo alembi sanathe kuima pamaso pa Mose chifukwa cha zilondazo; popeza panali zilonda pa alembi ndi pa Aejipito onse.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Tengani phulusa la ng'anjo lodzala manja; ndi Mose aliwaze kuthambo pamaso pa Farao.


Ndipo lidzakhala fumbi losalala padziko lonse la Ejipito, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoweta ngati zilonda zobuka ndi matuza, m'dziko lonse la Ejipito.


Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo.