Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 8:7 - Buku Lopatulika

Ndipo alembi anachita momwemo ndi matsenga ao, nakweretsa achule padziko la Ejipito.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo alembi anachita momwemo ndi matsenga ao, nakweretsa achule pa dziko la Ejipito.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma amatsenga aja nawonso adapanga ao achule ndipo adayamba kukwera pa mtunda.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma amatsenga anachita zinthu zomwezo mʼmatsenga awo. Iwonso anatulutsa achule mʼdziko lonse la Igupto.

Onani mutuwo



Eksodo 8:7
8 Mawu Ofanana  

Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao.


Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.


Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoze; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta.


chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.


Ndipo monga momwe Yane ndi Yambere anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana nacho choonadi; ndiwo anthu ovunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pachikhulupiriro.


Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.