Eksodo 8:5 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, pamtsinje, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse achule padziko la Ejipito.
Onani mutuwo
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, panyanja, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse achule pa dziko la Ejipito.
Onani mutuwo
Chauta adauzanso Mose kuti, “Uza Aroni kuti, ‘Uloze ndodo yako ku mitsinje, ku ngalande ndi ku zithaphwi ndipo pakhale achule pa dziko lonse la Aejipito.’ ”
Onani mutuwo
Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Loza ndodo yako ku mitsinje, ku ngalande ndi ku zithaphwi ndipo pakhale achule pa dziko lonse la Igupto.’ ”
Onani mutuwo