Ndi nsomba zili m'mtsinje zidzafa, ndi mtsinje idzanunkha; ndi Aejipito adzachita mtima useru ndi kumwa madzi a m'mtsinjemo.
Eksodo 7:24 - Buku Lopatulika Koma Aejipito onse anakumba m'mphepete mwa mtsinje kufuna madzi akumwa; pakuti sanakhoze kumwa madzi a m'mtsinjemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Aejipito onse anakumba m'mphepete mwa nyanja kufuna madzi akumwa; pakuti sanakhoze kumwa madzi a m'nyanjamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aejipito onse adayamba kukumba m'mbali mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sankathanso kumwa madzi a mu mtsinjewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu onse a ku Igupto anayamba kukumba mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sanathe kumwa madzi a mu mtsinjemo. |
Ndi nsomba zili m'mtsinje zidzafa, ndi mtsinje idzanunkha; ndi Aejipito adzachita mtima useru ndi kumwa madzi a m'mtsinjemo.