Eksodo 5:8 - Buku Lopatulika Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita ulesi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita chilezi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma chiŵerengero cha njerwa chikhale chonchija, monga momwe ankaumbira kale. Musaŵachepetsere ndi pang'ono pomwe, ngaulesi ameneŵa. Nchifukwa chake akulira nkumati, ‘Tiyeni tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma musawachepetsere chiwerengero cha njerwa chomwe munawalamulira kale kuti aziwumba. Iwowa ndi aulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, ‘Tiloleni tipite tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’ |
Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.
Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: chifukwa chake mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova.
Ndipo akapitao a ana a Israele anaona kuti kudawaipira, pamene ananena, Musamachepetsa njerwa zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake.