Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 106:41 - Buku Lopatulika

41 Ndipo anawapereka m'manja a amitundu; ndipo odana nao anachita ufumu pa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ndipo anawapereka m'manja a amitundu; ndipo odana nao anachita ufumu pa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Adaŵapereka kwa mitundu ina ya anthu, kotero kuti amene ankadana nawo, ndiwo amene ankaŵalamulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Iye anawapereka kwa anthu a mitundu ina, ndipo adani awo anawalamulira.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 106:41
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu; koma tisagwe m'dzanja la munthu.


Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kuchepsa gawo lako la chakudya, ndi kukupereka ku chifuniro cha iwo akudana nawe, kwa ana aakazi a Afilisti akuchita manyazi ndi njira yako yoipa.


Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.


ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.


Mtundu wa anthu umene simuudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;


chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.


Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.


Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu a ku Yuda, nati kwa Samisoni, Sudziwa kodi kuti Afilisti ndiwo akutilamulira ife? Nchiyani ichi watichitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandichitira ine ndawachitira iwo.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.


Koma ana a Israele anaonjezanso kuchita choipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Mowabu pa Israele, popeza anachita choipa pamaso pa Yehova.


Ndipo ana a Israele anatumikira Egiloni mfumu ya Mowabu zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele ndipo anawagulitsa m'dzanja la Kusani-Risataimu, mfumu ya Mesopotamiya; ndi ana a Israele anatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa