nalankhula nao monga mwa uphungu wa achinyamata, nati, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
Eksodo 5:5 - Buku Lopatulika Farao anatinso, Taonani, anthu a m'dziko ndiwo ambiri tsopano; ndipo inu muwapumitsa ku akatundu ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Farao anatinso, Taonani, anthu a m'dziko ndiwo ambiri tsopano; ndipo inu muwapumitsa ku akatundu ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Farao adapitirira kuŵauza kuti, “Anthu ameneŵa akuchulukana kwambiri tsopano. Bwanji inu mufuna kuŵaletsa kugwira ntchito yao?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndiponso Farao anati, “Taonani, anthuwa mʼdziko muno alipo ochuluka, ndipo inu mukuwaletsa kugwira ntchito.” |
nalankhula nao monga mwa uphungu wa achinyamata, nati, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzetsani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anatulukira kukazonda abale ake, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu Mwejipito ali kukantha Muhebri, wa abale ake.