Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 10:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzetsani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzetsani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ndiye kuti bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, kuyambira pano ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Abambo anga anakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzalichititsa kukhala lolemetsa kwambiri. Abambo anga anakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 10:11
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anyamatawo adakula naye pamodzi ananena naye, ndi kuti, Muzitero nao anthu awa adalankhula nanu, ndi kuti, Atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire ilo; muzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'chuuno mwa atate wanga.


Tsono Yerobowamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehobowamu tsiku lachitatu, monga mfumu idanena, ndi kuti Bweraninso kwa ine tsiku lachitatu.


Mukani tsopano, gwirani ntchito; pakuti sadzakupatsani udzu, koma muonetse chiwerengero chake cha njerwa.


Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsere chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.


Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse?


Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.


Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.


Ndipo lili nayo michira yofanana ndi ya chinkhanira ndi mbola; ndipo m'michira mwao muli mphamvu yao yakuipsa anthu miyezi isanu.


Ndipo mu utsimo mudatuluka dzombe padziko, ndipo analipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko zili ndi mphamvu.


Ndipo anapatsa ilo mphamvu si kuti likawaphe, komatu kuti likawazunze miyezi isanu; ndipo mazunzidwe ao anali ngati mazunzidwe a chinkhanira, pamene chiluma munthu.


Ndipo tsiku lija mudzafuula chifukwa cha mfumu yanu munadzisankhira nokha; koma Yehova sadzayankha inu tsiku lijalo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa