Potero anatsika, namira mu Yordani kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka.
Eksodo 4:7 - Buku Lopatulika Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lake pachifuwa pake; nalitulutsa pachifuwa pake, taonani, linasandukanso lomwe lakale. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lake pachifuwa pake; nalitulutsa pachifuwa pake, taonani, linasandukanso lomwe lakale. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adati, “Lipisenso m'malayamo dzanja lakolo.” Iye adalipisanso ndipo potulutsa, linali labwinobwino lopanda khate, koma lofanana ndi thupi lake lonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anati, “Tsopano pisanso dzanja lako mʼmalaya.” Mose anapisanso dzanja lakelo mʼmalaya ake ndipo atalitulutsa, linali labwinobwino, ngati thupi lake lonse. |
Potero anatsika, namira mu Yordani kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka.
Ndipo kudzatero, ngati sakhulupirira iwe, ndi kusamvera mau a chizindikiro choyamba, adzakhulupirira mau a chizindikiro chotsirizachi.
Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.
Ndipo m'mene analowa Iye m'mudzi wina, anakomana naye amuna khumi akhate, amene anaima kutali;
Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.