2 Mafumu 5:14 - Buku Lopatulika14 Potero anatsika, namira mu Yordani kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Potero anatsika, namira m'Yordani kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Motero Naamaniyo adapita ku Yordani, nakakhuvula m'madzimo kasanunkaŵiri, malinga ndi m'mene adaamuuzira munthu wa Mulungu uja. Pompo adachira ndipo thupi lake lidangoti see ngati la kamwana, choncho adakhala woyeretsedwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Choncho Naamani anapita ku Yorodani nakadzimiza mʼmadzimo kasanu nʼkawiri, monga momwe munthu wa Mulungu anamuwuzira. Thupi lake linakhalanso monga kale ndipo linakhala losalala ngati la kamnyamata. Onani mutuwo |