Ndipo anaika pomwepo mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba.
Eksodo 39:9 - Buku Lopatulika Chinakhala chaphwamphwa; anachiomba chapachifuwa chopindika; utali wake dzanja limodzi, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, chinakhala chopindika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chinakhala chaphwamphwa; anachiomba chapachifuwa chopindika; utali wake dzanja limodzi, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, chinakhala chopindika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kutalika kwake kwa chovala chapachifuwacho kunali masentimita 23, muufupi mwakenso masentimita 23, ndipo chinali chopinda paŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kutalika kwake kunali kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, chinali chopinda pawiri. |
Ndipo anaika pomwepo mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba.
Ndipo anaomba chapachifuwa, ntchito ya mmisiri, monga maombedwe ake a efodi; cha golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.