ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;
Eksodo 39:5 - Buku Lopatulika Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa chiombedwe chomwechi; wa golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa chiombedwe chomwechi; wa golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Panalinso lamba woluka mwaluso, womangira efodi, wolukira kumodzi ndi efodiyo. Lambayo nayenso anali wa nsalu yagolide, ndi wa nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso wa bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Lamba womangira efodi anali wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Anali nsalu imodzi ndi efodiyo, wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala, monga momwe Yehova analamulira Mose. |
ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;
Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa chiombedwe chomwecho, ndi woombera kumodzi, wagolide, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m'chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru;
Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolide, yolocha ngati malochedwe a chosindikizira, ndi maina a ana a Israele.
Ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa m'chuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpso zake.
Ndipo anamveka ndi malaya a m'kati, nammanga m'chuuno ndi mpango, namveka ndi mwinjiro, namveka ndi efodi, nammanga m'chuuno ndi mpango wa efodi nammanga nao pathupi pake.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate;
ndipo pakati pa zoikaponyalizo wina wonga Mwana wa Munthu atavala chofikira kumapazi ake, atamangira lamba lagolide pachifuwa.