Ndipo polowa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira polowa pake, wa ntchito yoomba, ngati polowa pa malaya otchinjiriza, pangang'ambike.
Eksodo 39:23 - Buku Lopatulika ndi pakati pake polowa mutu, ngati polowa pa malaya ochingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pake, pangang'ambike. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi pakati pake polowa mutu, ngati polowa pa malaya ochingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pake, pangang'ambike. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mkanjowo unali ndi popisa mutu, ndipo maonekedwe ake anali ngati popisa mutu pa malaya. M'mbali mwake kuzungulira, munali mosokerera bwino, kuti ungang'ambike. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mkanjowo unali ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo panali chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike. |
Ndipo polowa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira polowa pake, wa ntchito yoomba, ngati polowa pa malaya otchinjiriza, pangang'ambike.
Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.