Nsalu zisanu zilumikizane ina ndi inzake; ndi nsalu zisanu zina zilumikizane ina ndi inzake.
Eksodo 39:20 - Buku Lopatulika Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pake, pa mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pake, pa mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adapanganso mphete ziŵiri zagolide, nazilumikiza ku mbali yam'munsi, kutsogolo kwa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, pafupi ndi msoko, ndiponso pamwamba pa lamba woluka mwaluso uja wa efodiyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anapanga mphete zina ziwiri zagolide ndi kuzilumikiza kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi. |
Nsalu zisanu zilumikizane ina ndi inzake; ndi nsalu zisanu zina zilumikizane ina ndi inzake.
Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa chiombedwe chomwecho, ndi woombera kumodzi, wagolide, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pansonga ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake m'katimo, pa mbali ya kuefodi.
Ndipo anamanga chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose.