ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Eksodo 38:31 - Buku Lopatulika ndi makamwa a pabwalo pozungulira, ndi makamwa a ku chipata cha pabwalo, ndi zichiri zonse za chihema, ndi zichiri zonse za pabwalo pozungulira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi makamwa a pabwalo pozungulira, ndi makamwa a ku chipata cha pabwalo, ndi zichiri zonse za chihema, ndi zichiri zonse za pabwalo pozungulira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa masinde a bwalo lonse lozungulira, ndi zikhomo zonse za chihema cha Chauta ndi za bwalo lonse lozungulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero matsinde ozungulira bwalo ndiponso a pa chipata pake, ndi zikhomo zonse za tentiyo ndi matsinde a malo wozungulirapo. |
ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Zipangizo zonse za chihema, m'machitidwe ake onse, ndi zichiri zake zonse, ndi zichiri zonse za bwalo lake, zikhale zamkuwa.
Ndipo anapanga nao makamwa a pa khomo la chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi sefa wake amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe,
Ndipo anaomba zovala zakutumikira nazo ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, atumikire nazo m'malo opatulika, naomba zovala zopatulika za Aroni; monga Yehova adamuuza Mose.