Ndipo anaomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiira, ndi lofiirira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, naomberamo akerubi.
Eksodo 38:18 - Buku Lopatulika Ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo ndiyo ntchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake ndi kupingasa kwake mikono isanu, yolingana ndi nsalu zotchingira za pabwalo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo ndiyo ntchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake ndi kupingasa kwake mikono isanu, yolingana ndi nsalu zochingira za pabwalo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nsalu zochingira pa chipata cha ku bwalolo, zokongoletsedwa ndi zopetapeta, zinali zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, ndiponso za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Kutalika kwake kunali mamita asanu ndi anai, msinkhu wake unali masentimita 229 monga zochingira zake za bwalolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nsalu yotchinga ya pa chipata inali yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira, yofewa yosalala ndi yopangidwa ndi anthu aluso. Nsaluyo inali yotalika mamita asanu ndi anayi, molingana ndi nsalu zotchinga bwalo. Msinkhu wake unali masentimita 229, |
Ndipo anaomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiira, ndi lofiirira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, naomberamo akerubi.
Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.
Ndipo uziomba nsalu yotsekera pa khomo la hema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula.
Ndipo makamwa a nsichi anali amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva; ndi zokutira mitu yake zasiliva; ndi nsichi zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva.
Ndi nsichi zake zinali zinai, ndi makamwa ake anai, amkuwa; zokowera zake zasiliva, ndi zokutira mitu yake ndi mitanda yake zasiliva.