Nsalu zotchingira za pa mbali imodzi ya chipata nza mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu;
Eksodo 38:15 - Buku Lopatulika momwemonso pa mbali ina: pa mbali ino ndi pa mbali ina ya chipata cha pabwalo panali nsalu zotchingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 momwemonso pa mbali ina: pa mbali yino ndi pa mbali ina ya chipata cha pabwalo panali nsalu zochingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mbali inayo panali chimodzimodzi. Choncho pa mbali zonse ziŵirizo za chipata choloŵera ku bwalo chija, panali nsalu zochinga, zotalika mamita asanu ndi aŵiri, zokhala ndi nsanamira zitatu ndi masinde atatu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero polowera mʼbwalo panali nsalu yotchinga ya mamita asanu ndi awiri pamodzi ndi mizati itatu ndi matsinde atatu. |
Nsalu zotchingira za pa mbali imodzi ya chipata nza mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu;