ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Eksodo 38:12 - Buku Lopatulika Ndi pa mbali ya kumadzulo panali nsalu zotchingira za mikono makumi asanu, nsichi zake khumi, ndi makamwa ake khumi; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi pa mbali ya kumadzulo panali nsalu zochingira za mikono makumi asanu, nsichi zake khumi, ndi makamwa ake khumi; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mbali yakuzambwe panali nsalu zochingira, kutalika kwake mamita 23, ndi nsanamira zake khumi ndi masinde khumi. Ngoŵe zake ndiponso mitanda yake zinali zasiliva. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mbali yakumadzulo inali yotalika mamita 23 ndipo inali ndi nsalu yotchinga, mizati khumi ndi matsinde khumi. Inalinso ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. |
ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Ndi pa mbali ya kumpoto mikono zana limodzi, nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ake makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva.