Anapanganso akerubi awiri agolide; anachita kuwasula mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo;
Eksodo 37:8 - Buku Lopatulika kerubi mmodzi pa mbali yake imodzi, ndi kerubi wina pa mbali yake ina; anapanga akerubi ochokera m'chotetezerapo, pa mathungo ake awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kerubi mmodzi pa mbali yake imodzi, ndi kerubi wina pa mbali yake ina; anapanga akerubi ochokera m'chotetezerapo, pa mathungo ake awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa wina uku wina uku. Adaŵapangira kumodzi ndi chivundikirocho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anapanga kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa anawapangira limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo. |
Anapanganso akerubi awiri agolide; anachita kuwasula mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo;
Ndipo akerubi anafunyulira mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zopenyana; zinapenya kuchotetezerapo nkhope zao.