Analipangiranso mitanda pozungulirapo, yoyesa chikhato m'kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira anapangirapo mkombero wagolide.
Eksodo 37:13 - Buku Lopatulika Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide, naika mphetezo pangodya zake zinai zokhala pa miyendo yake inai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide, naika mphetezo pangodya zake zinai zokhala pa miyendo yake inai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka adapanganso mphete zinai zagolide za tebulolo, naziika pa ngodya zinai ku miyendo ya tebulolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anapanga mphete zinayi zagolide ndipo anazilumikiza ku ngodya zake zinayi, kumene kunali miyendo yake inayi. |
Analipangiranso mitanda pozungulirapo, yoyesa chikhato m'kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira anapangirapo mkombero wagolide.