Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wao.
Eksodo 36:16 - Buku Lopatulika Ndipo anamanga pamodzi nsalu zisanu pazokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pazokha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamanga pamodzi nsalu zisanu pa zokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pa zokha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adasokerera nsalu zisanu nkukhala chinsalu chimodzi, ndipo nsalu zinazo zisanu ndi imodzi, adazisokereranso kuti zikhale chinsalu chimodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo analumikiza nsalu zisanu kukhala nsalu imodzi ndipo nsalu zinazo zisanu ndi imodzi, analumikizanso kukhala nsalu imodzinso. |
Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wao.
Ndipo anapanga magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo, ya chilumikizano, naika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano china.