Ndipo uziika magango a nsalu ya madzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi, ku mkawo wa chilumikizano; nuchite momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
Eksodo 36:11 - Buku Lopatulika Ndipo anaika magango ansalu yamadzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi ku mkawo wa chilumikizano; nachita momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano chachiwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaika magango ansalu yamadzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi ku mkawo wa chilumikizano; nachita momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano chachiwiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake adasoka magonga a tinsalu tobiriŵira m'mphepete mwa chimodzi kubwalo kwake, ndipo adachitanso chimodzimodzi ndi chinacho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anapanga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo. |
Ndipo uziika magango a nsalu ya madzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi, ku mkawo wa chilumikizano; nuchite momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
Ndipo analumikiza nsalu zisanu ina ndi inzake; nalumikiza nsalu zisanu zina ina ndi inzake.
Anaika magango makumi asanu pansalu imodzi, naikanso magango makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; magango anakomanizana lina ndi linzake.