Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha, Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kunka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono.
Eksodo 33:8 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, pakutuluka Mose kunka ku chihemacho kuti anthu onse anaimirira, nakhala chilili, munthu yense pakhomo pa hema wake, nachita chidwi pa Mose, kufikira atalowa m'chihemacho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, pakutuluka Mose kunka ku chihemacho kuti anthu onse anaimirira, nakhala chilili, munthu yense pakhomo pa hema wake, nachita chidwi pa Mose, kufikira atalowa m'chihemacho. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi zonse Mose akamapita kuchihemako, anthu onse ankaimirira. Tsono aliyense ankangoimirira pakhomo pa hema lake, namayang'ana Moseyo mpaka ataloŵa m'chihema chokumaniranako ndi Chauta chija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo nthawi ina iliyonse imene Mose amapita ku tenti anthu onse amanyamuka ndi kuyimirira pa makomo amatenti awo, kumuyangʼana Mose mpaka atalowa mu tentimo. |
Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha, Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kunka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono.
Ndipo kunali, pakulowa Mose m'chihemacho, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa chihemacho; ndipo Yehova analankhula ndi Mose.
Potero anakwera kuchokera pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu, ndipo Datani ndi Abiramu anatuluka, naima pakhomo pa mahema ao, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna, ndi makanda ao.