Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina chifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo.
Eksodo 3:13 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israele, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? Ndikanena nao chiyani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israele, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? Ndikanena nao chiyani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adayankha kuti, “Tsono ine ndikapita kwa Aisraelewo kukaŵauza kuti Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu, iwowo akakandifunsa kuti, ‘Dzina lake ndani?’ Ndiye ineyo ndikaŵauze chiyani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti ‘Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?” |
Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina chifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo.
Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo mu Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.
Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.
Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo.
Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumikire m'chipululu; koma, taona, sunamvere ndi pano.
Ndani anakwera kumwamba natsikanso? Ndani wakundika nafumbata mphepo? Ndani wamanga madzi m'malaya ake? Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko? Dzina lake ndani? Dzina la mwanake ndani? Kapena udziwa.
Chifukwa chake anthu anga adzadziwa dzina langa; chifukwa chake tsiku limenelo iwo adzadziwa kuti Ine ndine amene ndinena; taonani, ndine pano.
Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele.
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.
Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.
Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.
Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.
Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Dzina lanu ndani, kuti, atachitika mau anu, tikuchitireni ulemu.
Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wake ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ake ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunse uko achokera kapena sanandiuzenso dzina lake;