Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Eksodo 29:6 - Buku Lopatulika ndipo uike nduwira pamutu pake, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo uike nduwira pamutu pake, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Umuveke nduŵira kumutu kwake, ndi duŵa lopatulika lija panduŵirapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Umuveke nduwira kumutu, ndiponso uyike chizindikiro chopatulika chija pa nduwirayo. |
Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Asatuluke m'malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wake; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wake ali pa iye; Ine ndine Yehova.
Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.
Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pake. Naika nduwira yoyera pamutu pake, namveka ndi zovala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo.