Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake.
Eksodo 28:7 - Buku Lopatulika Akhale nazo zapamapewa ziwiri zomangika ku nsonga zake ziwiri, kuti amangike nazo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akhale nazo zapamapewa ziwiri zomangika ku nsonga zake ziwiri, kuti amangike nazo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Idzakhale ndi tizikwewo tam'mapewa tiŵiri tosokerera ku nsonga zake ziŵiri, tomangira efodiyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Efodiyo ikhale ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga. |
Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake.
Naombe efodi ndi golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri.
Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa chiombedwe chomwecho, ndi woombera kumodzi, wagolide, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Ndi nsonga zake ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m'tsogolo mwake.