Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsalu zotchingira za mikono makumi asanu; nsichi zake zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi.
Eksodo 27:13 - Buku Lopatulika Ndipo m'kupingasa kwake kwa bwalo pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mukhale mikono makumi asanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'kupingasa kwake kwa bwalo pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mukhale mikono makumi asanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chakuvuma, komwe kuli chipata chake, bwalolo likhalenso mamita 23 muufupi mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mbali yakummawa, kotulukira dzuwa, kutalika kwa bwalo kukhale mamita 23. |
Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsalu zotchingira za mikono makumi asanu; nsichi zake zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi.
Ndi nsalu zotchingira za pa mbali imodzi ya kuchipata zikhale za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu.