Ndi mkono wa pa mbali ino, ndi mkono wa pa mbali inzake, wakutsalira mu utali wake wa nsalu zophimbazo, itchinge pambali zake za chihemacho, mbali ino ndi mbali ina, kumphimba.
Eksodo 26:8 - Buku Lopatulika Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muutali mwake nsalu iliyonse ikhale mamita 14, ndipo muufupi mwake pafupi mamita aŵiri. Zonsezo zikhale zofanana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nsalu zonse khumi ndi imodzi zikhale zofanana. Mulitali mwake mukhale mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake mukhale mamita awiri. |
Ndi mkono wa pa mbali ino, ndi mkono wa pa mbali inzake, wakutsalira mu utali wake wa nsalu zophimbazo, itchinge pambali zake za chihemacho, mbali ino ndi mbali ina, kumphimba.
Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu zonse zikhale za muyeso umodzi.
Ndipo uziomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale chophimba pamwamba pa chihema; uziomba nsalu khumi ndi imodzi.
Nuzisoka pamodzi nsalu zisanu pazokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pazokha, nupinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo pa khomo la hema.