Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati chagwirira ntchito yakulipira, chadzera kulipira kwake.
Eksodo 22:16 - Buku Lopatulika Munthu akanyenga namwali wosapalidwa ubwenzi, nakagona naye, alipetu kuti akhale mkazi wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munthu akanyenga namwali wosapalidwa ubwenzi, nakagona naye, alipetu kuti akhale mkazi wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Munthu akanyenga namwali wosadziŵa mwamuna, yemwe sanatomeredwe, nagona naye, alipire chiwongo, ndipo amkwatire. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ngati munthu anyenga namwali wosadziwa mwamuna amene sanapalidwe ubwenzi ndi kugona naye, munthuyo ayenera kulipira malowolo ndipo adzakhala mkazi wake. |
Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati chagwirira ntchito yakulipira, chadzera kulipira kwake.
Njira ya mphungu m'mlengalenga, njira ya njoka pamwala, njira ya ngalawa pakati pa nyanja, njira ya mwamuna ndi namwali.
Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.