Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Taonanitu, Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: lowanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana. Ndipo Abramu anamvera mau a Sarai.
Eksodo 21:4 - Buku Lopatulika Akampatsa mkazi mbuye wake, ndipo akambalira ana aamuna ndi aakazi, mkaziyo ndi ana ake azikhala a mbuye wake, ndipo azituluka ali yekha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akampatsa mkazi mbuye wake, ndipo akambalira ana aamuna ndi aakazi, mkaziyo ndi ana ake azikhala a mbuye wake, ndipo azituluka ali yekha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati mbuyake adampatsa mkazi, ndipo adamubalirapo ana aamuna kapena aakazi, mkaziyo pamodzi ndi anawo onse ndi a mbuyakeyo. Tsono mwamuna yekhayo ndiye adzachoke. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati bwana wake amupatsa mkazi ndipo mkaziyo anabereka ana aamuna kapena aakazi, mkazi ndi anawo adzakhala a bwanayo ndipo mwamuna yekhayo ndiye adzamasulidwe. |
Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Taonanitu, Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: lowanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana. Ndipo Abramu anamvera mau a Sarai.
Azidulidwatu amene abadwa m'nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m'thupi mwako pangano losatha.
Koma mnyamatayo akanenetsa, Ndikonda mbuye wanga, mkazi wanga, ndi ana anga; sindituluka waufulu;