Eksodo 21:24 - Buku Lopatulika diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, mkono kulipa mkono, phazi kulipa phazi. |
Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.
Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.
Ndipo diso lanu lisachite chifundo, moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi.
popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.
Ndipo Samuele anati, Monga lupanga lako linachititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samuele anamdula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.