Koma munthu akachita dala pa mnzake, kumupha monyenga; uzimchotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe.
Eksodo 21:15 - Buku Lopatulika Munthu wakukantha atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munthu wakukantha atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Munthu aliyense amene amenya bambo wake kapena mai wake, aphedwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Munthu aliyense amene amenya abambo ake kapena mayi ake ayenera kuphedwa. |
Koma munthu akachita dala pa mnzake, kumupha monyenga; uzimchotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe.
Iye wakuba munthu, angakhale wamgulitsa, kapena akampeza m'dzanja lake, aphedwe ndithu.
Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.
podziwa ichi, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osaweruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao,