Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m'phiri, musakhudza malire ake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;
Eksodo 19:23 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m'phiri la Sinai; pakuti Inu mwatichenjeza, ndi kuti, Lemba malire m'phirimo, ndi kulipatula. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m'phiri la Sinai; pakuti Inu mwatichenjeza, ndi kuti, Lemba malire m'phirimo, ndi kulipatula. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adayankha Chauta kuti, “Anthuwo sangakwere ai, chifukwa mudachenjezeratu kuti, ‘Mulembe malire kuzungulira phirilo, ndipo mulipatule kuti likhale loyera.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anati kwa Yehova, “Anthu sangakwere phiri la Sinai chifukwa inu munatichenjeza. Lembani malire kuzungulira phiri ndipo mulipatule kuti likhale loyera.” |
Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m'phiri, musakhudza malire ake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;
Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika; nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule.