Eksodo 10:11 - Buku Lopatulika Chotero ai, mukani tsopano, inu amuna aakulu, tumikirani Yehova pakuti ichi muchifuna. Ndipo anawapirikitsa pamaso pa Farao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chotero ai, mukani tsopano, inu amuna akulu, tumikirani Yehova pakuti ichi muchifuna. Ndipo anawapirikitsa pamaso pa Farao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ai! Inu, amuna nokhanu, ndiye mupite mukapembedze Chauta, popeza kuti ndi zimene mukufuna.” Atangomveka mau ameneŵa, Mose ndi Aroni adapirikitsidwa pamaso pa Farao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndakana! Amuna okha ndiwo apite ndi kukapembedza Yehova pakuti izi ndi zimene mwakhala mukupempha.” Kenaka Mose ndi Aaroni anathamangitsidwa pamaso pa Farao. |
Ndipo ananena nao, Momwemo, Yehova akhale nanu ngati ndilola inu ndi ana aang'ono anu mumuke; chenjerani pakuti pali choipa pamaso panu.
Ndipo Farao ananena naye, Choka pano, uzichenjera usaonenso nkhope yanga; pakuti tsiku limene uonanso nkhope yanga udzafa.
Ndipo mfumu ya Aejipito inanena nao, Inu, Mose ndi Aroni, chifukwa ninji mumasulira anthu ntchito zao? Mukani ku akatundu anu.