Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana aamunawo akhale ndi moyo?
Eksodo 1:19 - Buku Lopatulika Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Azamba aja adayankha kuti “Azimai achihebri safanafana ndi azimai achiejipito. Iwo ngamphamvu, amati mzamba asanafike, mwana amakhala atabadwa kale.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Azambawo anamuyankha Farao kuti, “Amayi a Chihebri sali ngati amayi a Chiigupto; Iwo ndi amphamvu ndipo amachira azamba asanafike.” |
Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana aamunawo akhale ndi moyo?
Potero Mulungu anawachitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu.
Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira ntchito, ninena nane, Asadziwe munthu aliyense kanthu za ntchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.